Isaiah 34:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Lupanga langa lakhutiratu kumwamba. Si ili likutsika kudzalanga Aedomu, anthu amene ndatsimikiza kuti ndiŵaononga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti lupanga langa lakhuta kumwamba; taonani, lidzatsikira pa Edomu, ndi pa anthu amene ndawatemberera, kuti aweruzidwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Lupanga langa lakhutiratu magazi kumwamba; taonani, likutsika kudzalanga anthu a ku Edomu, anthu amene ndawawononga kotheratu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti lupanga langa lakhuta kumwamba; taonani, lidzatsikira pa Edomu, ndi pa anthu amene ndawatemberera, kuti aweruzidwe.