Isaiah 34:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Lupanga la Chauta lakhuta magazi, ndipo lakutidwa ndi mafuta. Magazi ake a anaankhosa ndi a mbuzi, ndipo mafuta ake a ku impso za nkhosa zamphongo. Pakuti Chauta ali ndi nsembe mu mzinda wa Bozira, ndiye kuti kuphedwa kwa anthu ambiri m'dziko la Edomu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Lupanga la Yehova lakhuta ndi mwazi, lanona ndi mafuta ndi mwazi wa anaankhosa, ndi mbuzi, ndi mafuta a impso ya nkhosa zamphongo; pakuti Yehova ali ndi nsembe m'Bozira, ndi ophedwa ambiri m'dziko la Edomu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lupanga la Yehova lakhuta magazi, lakutidwa ndi mafuta; magazi a ana ankhosa onenepa ndi ambuzi, mafuta a ku impsyo za nkhosa zazimuna. Pakuti Yehova ali ndi nsembe mu Bozira ndiko kuphedwa kwa anthu ambiri mʼdziko la Edomu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Lupanga la Yehova lakhuta ndi mwazi, lanona ndi mafuta ndi mwazi wa ana a nkhosa, ndi mbuzi, ndi mafuta a imso ya nkhosa zamphongo; pakuti Yehova ali ndi nsembe m'Bozira, ndi ophedwa ambiri m'dziko la Edomu.