Isaiah 35:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzikolo lidzakhala ndi maluŵa ochuluka ongodzimerera okha. Lidzasangalala ndi kufuula ndi chimwemwe. Lidzakhala ndi ulemerero wonga wa mapiri a ku Lebanoni, maonekedwe ake adzakhala okongola ngati a ku Karimele ndi Saroni. Aliyense adzaona ulemerero wa Chauta ndi ukulu wa Mulungu wathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Lidzaphuka mochuluka ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuimba; lidzapatsidwa ulemerero wa Lebanoni, ndi ukulu wa Karimele ndi Saroni; anthuwo adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wake wa Mulungu wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzikolo lidzakhala ndi maluwa ochuluka lidzasangalala kwambiri ndi kufuwula mwachimwemwe. Lidzakhala ndi ulemerero monga wa ku mapiri a ku Lebanoni, maonekedwe ake wokongola adzakhala ngati a ku Karimeli ndi a ku Saroni. Aliyense adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wa Mulungu wathu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Lidzaphuka mocuruka ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuyimba; lidzapatsidwa ulemerero wa Lebano, ndi ukuru wa Karimeli ndi Saroni; anthuwo adzaona ulemerero wa Yehova, ukuru wace wa Mulungu wathu.