Isaiah 35:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Opunduka adzalumpha ngati mphoyo, ndipo osalankhula adzaimba mokondwa. Akasupe adzatumphuka m'chipululu, ndipo mitsinje idzayenda m'dziko louma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba; pakuti m'chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m'dziko loti see.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu olumala adzalumpha ngati mbawala, ndipo osayankhula adzayimba mokondwera. Akasupe adzatumphuka mʼchipululu ndipo mitsinje idzayenda mʼdziko lowuma,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilume la wosalankhula lidzayimba; pakuti m'cipululu madzi adzaturuka, ndi mitsinje m'dziko loti se.