Isaiah 35:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumeneko kudzakhala mseu waukulu wotchedwa “Mseu Wopatulika.” Ochimwa sadzayendamo, ndipo zitsilu sizidzasokera m'menemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzakhala khwalala kumeneko, ndi njira, ndipo idzatchedwa njira yopatulika; odetsedwa sadzapita m'menemo; koma Iye adzakhala nao oyenda m'njira, ngakhale opusa, sadzasochera m'menemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo kumeneko kudzakhala msewu waukulu; ndipo udzatchedwa Msewu Wopatulika. Anthu odetsedwa sadzayendamo mʼmenemo; zitsiru sizidzasochera mʼmenemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzakhala khwalala kumeneko, ndi njira, ndipo idzachedwa njira yopatulika; audio sadzapita m'menemo; koma Iye adzakhala nao oyenda m'njira, ngakhale opusa, sadzasocera m'menemo.