Isaiah 36:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka cha 14 cha ufumu wa Hezekiya, mfumu ya ku Yuda, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya adathira nkhondo mizinda yonse yamalinga ya ku Yuda, nailanda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma panali chaka chakhumi ndi chinai cha mfumu Hezekiya, Senakeribu, mfumu ya Asiriya anadza, nathira nkhondo pa midzi ya malinga yonse ya Yuda, nailanda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chaka cha khumi ndi chinayi cha ulamuliro wa Mfumu Hezekiya, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anathira nkhondo mizinda yonse yotetezedwa ya ku Yuda, nayilanda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma panali caka cakhumi ndi cinai ca mfumu Hezekiya, Sanakeribu, mfumu ya Asuri anadza, nathira nkhondo pa midzi ya malinga yonse ya Yuda, nailanda.