Isaiah 36:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiponso kodi sukudziŵa kuti ndi Chauta amene wandibweretsa kuno, ndidzathire nkhondo dziko lino ndi kuliwononga? Chautayo ndiye adachita kundiwuza kuti ndilimbane nalo ndi kuliwononga dziko lino.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ine tsopano, kodi ndafika opanda Yehova kudzamenyana ndi dziko ili, kudzalipasula? Yehova anati kwa ine, Kwera, ndi kumenyana ndi dziko ili, ndi kulipasula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuwonjezera pamenepa, kodi ine ndabwera kudzathira nkhondo ndi kuwononga dziko lino popanda chilolezo cha Yehova? Yehova mwini ndiye anandiwuza kuti ndidzathire nkhondo ndi kuwononga dziko lino.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ine tsopano, kodi ndafika opanda Yehova kudzamenyana ndi dziko ili, kudzalipasula? Yehova anati kwa ine, Kwera, ndi kumenyana ndi dziko ili, ndi kulipasula.