Isaiah 36:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Eliyakimu, Sebina ndi Yowa adauza kazembeyo kuti, “Pepani, mutilankhule m'Chiaramu atumiki anufe, poti timachimvetsa. Musatilankhule m'Chiyuda, pakuti anthu onse ali pakhomaŵa alikumva.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Eliyakimu, ndi Sebina, ndi Yowa, anati kwa kazembeyo, Nenanitu kwa atumiki anu m'chinenero cha Aramu; pakuti ife tichimva; ndipo musanene kwa ife m'Chiyuda, m'makutu a anthu amene ali palinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Eliyakimu, Sebina ndi Yowa anawuza kazembeyo kuti, “Chonde yankhulani kwa atumiki anufe mʼChiaramu, popeza timachimva. Musayankhule nafe mu Chihebri kuopa kuti anthu onse amene ali pa khomapa angamve.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Eliakimu, ndi Sebina, ndi Yoaki, anati kwa kazembeyo, Nenanitu kwa atumiki anu m'cinenero ca Aramu; pakuti ife ticimva; ndipo musanene kwa ife m'Ciyuda, m'makutu a anthu amene ali palinga.