Isaiah 36:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma kazembe uja adati, “Kodi mukuganiza kuti mfumu yanga idandituma kuti ndilankhule mau ameneŵa kwa inu nokha ndi kwa mfumu yanu basi? Iyai, ndikulankhulanso kwa anthu amene akhala pakhomowo, amene adzayenera kudya ndoŵe yao yomwe ndi kumwa mkodzo wao womwe, monga momwe mudzachitire inuyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kazembeyo anati, Kodi mbuyanga ananditumiza ine kwa mbuyako ndi kwa iwe kunena mau amenewa? Kodi iye sananditumize adye ndowe zaozao, ndi kumwa madzi aoao ndi inu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma kazembeyo anayankha kuti, “Kodi mbuye wanga wandituma kuti ndidzanene zinthu izi kwa mbuye wanu yekha ndi inu nokha basi? Ayi, komanso kwa anthu amene akhala pa khomawa. Iwowa adzadya chimbudzi chawo chomwe ndi kumwa mkodzo wawo womwe monga momwe mudzachitire inuyonso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kazembeyo anati, Kodi mbuyanga ananditumiza ine kwa mbuyako ndi kwa iwe kunena mau amenewa? kodi iye sananditumiza ine kwa amuna okhala palinga, kuti adye ndowe zao zao, ndi kumwa madzi ao ao ndi inu?