Isaiah 36:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asakukakamizeni kuti mudalire Chauta pokuuzani kuti mosapeneka konse Chauta wanuyo adzakupulumutsani, ndipo kuti mfumu ya ku Asiriya sidzalanda mzinda wanuwu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ngakhale musaleke Hezekiya akhulupiritse inu kwa Yehova, ndi kunena, Yehova adzatipulumutsa ndithu; mudzi uwu sudzaperekedwa m'manja mwa mfumu ya Asiriya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hezekiya asakukakamizeni kudalira Yehova ndi mawu akuti, ‘Ndithu, Yehova adzatipulumutsa; ndipo sadzapereka mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ngakhale musaleke Hezekiya akhulupiritse inu kwa Yehova, ndi kunena, Yehova adzatipulumutsa ndithu; mudzi uwu sudzaperekedwa m'manja mwa mfumu ya Asuri.