Isaiah 36:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye inu chenjerani, Hezekiya asakupusitseni pokuuzani kuti Chauta adzakupulumutsani. Mwa milungu ya anthu a mitundu ina, kodi alipo ndi mmodzi yemwe amene adapulumutsapo dziko lake kwa mfumu ya ku Asiriya?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chenjerani angakukopeni inu Hezekiya, ndi kuti, Yehova adzatipulumutsa ife. Kodi milungu iliyonse ya amitundu inapulumutsa dziko lao m'manja mwa mfumu ya ku Asiriya?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu musalole kuti Hezekiya akusocheretseni pamene iye akuti, ‘Yehova adzatipulumutsa.’ Kodi alipo mulungu wa anthu a mtundu wina amene anapulumutsa dziko lake mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cenjerani angakukopeni inu Hezekiya, ndi kuti, Yehova adzatipulumutsa ife. Kodi milungu iri yonse ya amitundu inapulumutsa dziko lao m'manja mwa mfumu ya ku Asuri?