Isaiah 36:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake mfumu ya ku Asiriyayo idatuma kazembe wake wankhondo kuchokera ku Lakisi, kuti apite ndi gulu lalikulu lankhondo kwa Hezekiya ku Yerusalemu. Tsono kazembeyo adaima pafupi ndi ngalande yamadzi yochokera ku dziŵe lakumtunda, pa mseu waukulu wopita ku malo a mmisiri woyeretsa nsalu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu ya Asiriya inatumiza kazembe kuchokera pa Lakisi, kunka ku Yerusalemu, kwa mfumu Hezekiya, ndi nkhondo yambiri. Ndipo iye anaima chifupi ndi mcherenje wa thamanda la kumtunda, m'khwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsalu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mfumu ya ku Asiriya inatuma kazembe wake wankhondo pamodzi ndi gulu lalikulu lankhondo kuchokera ku Lakisi kupita kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Tsono kazembeyo anayima pafupi ndi ngalande yamadzi yochokera ku Dziwe lakumtunda pa msewu wopita ku malo a munda wa mmisiri wochapa zovala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu ya Asuri inatumiza kazembe kucokera pa Lakisi, kunka ku Yerusalemu, kwa mfumu Hezekiya, ndi nkhondo yambiri. Ndipo iye anaima cifupi ndi mcerenje wa thamanda la kumtunda, m'khwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsaru.