Isaiah 36:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ndi iti mwa milungu ya maikoŵa imene idapulumutsapo maiko ake kwa mfumu yathu, kuti inu muziti Chauta nkupulumutsa Yerusalemu kwa mfumu yathuyo?’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa milungu yonse ya maiko awa, inapulumutsa dziko lao m'manja mwanga ndi iti, kuti Yehova adzapulumutsa Yerusalemu m'manja mwanga?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi ndi milungu iti mwa milungu yonse ya mayiko awa amene anapulumutsa dziko lake mʼdzanja? Nanga tsono Yehova adzapulumutsa Yerusalemu mʼdzanja langa motani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa milungu yonse ya maiko awa, inapulumutsa dziko lao m'manja mwanga ndi iti, kuti Yehova adzapulumutsa Yerusalemu m'manja mwanga?