Isaiah 36:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya amene ankayang'anira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo, ndi Yowa mwana wa Asafu, wolemba zochitika, adang'amba zovala zao mwachisoni, ndipo adapita kwa mfumu Hezekiya nakamuuza zimene kazembe wa ku Asiriya uja adaalankhula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anafika Eliyakimu, mwana wa Hilikiya, amene anali wapanyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi Yowa, mwana wa Asafu, mkumbutsi, kwa Hezekiya ndi zovala zao zong'ambika, namuuza iye mau a kazembeyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo anthu atatu aja Eliyakimu, mwana wa Hilikiya amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu; Sebina mlembi wa bwalo; ndi Yowa, mwana wa Asafu mlembi wa zochitika anapita kwa Hezekiya atangʼamba zovala zawo ndipo anamuwuza zonse zimene anayankhula kazembe uja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anafika Eliakimu, mwana wa Hilikiya, amene anali wapanyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi Yoaki, mwana wa Asafu, mkumbutsi, kwa Hezekiya ndi zobvala zao zong'ambika, namuuza iye mau a kazembeyo.