Isaiah 36:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu atatu adatuluka mu mzinda nakakumana naye. Anthu ake ndi aŵa: mkulu woyang'anira nyumba ya mfumu, dzina lake Eliyakimu mwana wa Hilikiya, Sebina mlembi wa bwalo, ndi Yowa mwana wa Asafu, wolemba zochitika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamtulukira Eliyakimu, mwana wa Hilikiya, amene anali wapanyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi Yowa, mwana wa Asafu, mkumbutsi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Panali anthu atatu. Woyamba anali Eliyakimu mwana wa Hilikiya komanso ndiye woyangʼanira nyumba ya mfumu. Wachiwiri anali Sebina amene anali mlembi wa bwalo; ndipo wachitatu anali Yowa mwana wa Asafu komanso anali wolemba zochitika. Anthu awa anatuluka kukakumana ndi kazembe wa ankhondo uja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamturukira Eliakimu, mwana wa Hilikiya, amene anali wapanyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi Yoaki, mwana wa Asafu, mkumbutsi.