Isaiah 36:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kazembe wankhondo uja adaŵauza kuti akanene kwa Hezekiya mau aŵa: “Mfumu yaikulu, mfumu ya ku Asiriya ikuti, ‘Chimene chikulimbitsa chikhulupiriro chako motere nchiyani?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kazembeyo anati kwa iwo, Nenani inu tsopano kwa Hezekiya, Itero mfumu yaikulu, mfumu ya Asiriya, Kodi chikhulupiriro ichi nchotani, uchikhulupirira iwe?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kazembe wa ankhondo anawawuza kuti, “Kamuwuzeni Hezekiya kuti, “Mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya ikunena kuti, Kodi chikukulimbitsa mtima ndi chiyani?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kazembeyo anati kwa iwo, Nenani inu tsopano kwa Hezekiya, Itero mfumu yaikuru, mfumu ya Asuri, Kodi cikhulupiriro ici ncotani, ucikhulupirira iwe?