Isaiah 36:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Makamaka ukuyembekeza kuti Ejipito adzakuthandiza. Koma kuteroko kuli ngati kukhulupirira bango lothyoka limene litha kum'baya munthu m'manja ataliyesa ndodo yoyendera. Ndimo m'mene mfumu ya ku Ejipito imamchitira aliyense woidalira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, ukhulupirira ndodo yabango iyi yophwanyika, kunena Ejipito; imene munthu akaitsamira, idzalowa m'dzanja mwake, ndi kulipyoza; momwemo Farao, mfumu ya Aejipito, kwa onse amene amkhulupirira iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taona tsono, iwe ukudalira Igupto, bango lothyokalo, limene limalasa mʼmanja mwa munthu ngati waliyesa ndodo yoyendera! Umo ndi mmene Farao mfumu ya ku Igupto imachitira aliyense amene akuyidalira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, ukhulupirira ndodo yabango iyi yophwanyika, kunena Aigupto; imene munthu akaitsamira, idzalowa m'dzanja mwace, ndi kulipyoza; momwemo Farao, mfumu ya Aigupto, kwa onse amene amkhulupirira iye.