Isaiah 36:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kapena undiwuza kuti mumakhulupirira Chauta Mulungu wanu.” Kodi si Mulungu yemweyo amene akachisi ake ndi maguwa ake, Hezekiya adaŵathetsa, nauza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, “Muzipembedza pa guwa ili la ku Yerusalemu?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ukanena kwa ine, Ife tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; kodi si ndiye amene Hezekiya wachotsa misanje yake ndi maguwa ake a nsembe, nati kwa Yuda, ndi kwa Yerusalemu, Inu mudzapembedzera patsogolo pa guwa la nsembe ili?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati ukunena kwa ine kuti, ‘Ife tikudalira Yehova Mulungu wathu,’ kodi si Mulungu yemweyo amene nyumba zake ndi maguwa ake, Hezekiya anachotsa, nawuza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, ‘Muzipembedza pa guwa lansembe ili?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ukanena kwa ine, Ife tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; kodi si ndiye amene Hezekiya wacotsa misanje yace ndi maguwa ace a nsembe, nati kwa Yuda, ndi kwa Yerusalemu, Inu mudzapembedzera patsogolo pa suwa la nsembe ili?