Isaiah 36:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tiye tsono utembezane ndi mbuye wanga, mfumu ya ku Asiriya: Ndidzakupatsa akavalo okwanira zikwi ziŵiri ngati iwe ungathe kupeza anthu ake okwerapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake upereketu zikole kwa mbuyanga, mfumu ya Asiriya, ndipo ine ndidzakupatsa iwe akavalo zikwi ziwiri, ngati iwe udzaona okwerapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo tsopano bwera udzakambirane ndi mbuye wanga, mfumu ya ku Asiriya: Ine ndidzakupatsa akavalo 2,000 ngati ungathe kupeza okwerapo!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace upereketu zikole kwa mbuyanga, mfumu ya Asuri, ndipo ine ndidzakupatsa iwe akavalo zikwi ziwiri, ngati iwe udzaona okwerapo.