Isaiah 37:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wakhala ulikumva zimene mafumu a ku Asiriya adaŵachita maiko onse, kuti adaŵaononga kotheratu. Tsono iweyo ndiye nkupulumuka?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, iwe wamva chimene mafumu a Asiriya anachitira maiko onse, ndi kuwapasula konse; ndipo kodi iwe udzapulumutsidwa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndithudi iwe unamva zimene mafumu a ku Asiriya akhala akuchitira mayiko onse. Iwo anawawononga kotheratu. Tsono iwe ndiye ndi kupulumuka?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, iwe wamva cimene mafumu a Asuri anacitira maiko onse, ndi kuwapasula konse; ndipo kodi iwe udzapulumutsidwa?