Isaiah 37:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Hezekiya adalandira kalata kwa amithenga aja, naiŵerenga. Pomwepo adapita ku Nyumba ya Chauta, naika kalatayo m'menemo pamaso pa Chauta,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hezekiya analandira kalatayo m'manja mwa mithengayo, namuwerenga; ndipo Hezekiya anakwera kunka kunyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hezekiya analandira kalata kwa amithenga nayiwerenga pomwepo. Hezekiya anapita ku Nyumba ya Yehova ndipo anayika kalatayo pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hezekiya analandira kalatayo m'manja mwa mithengayo, namuwerenga; ndipo Hezekiya anakwera kunka ku nyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova.