Isaiah 37:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Inu Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pamwamba pa akerubi, inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lonse lapansi. Mudalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, amene mukhala pa akerubi, Inu ndinu Mulungu, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pakati pa akerubi, Inu nokha ndiye Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, amene mukhala pa akerubi, Inu ndinu Mulungu, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.