Isaiah 37:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatentha milungu yao imene siinali milungu konse, koma mafano amitengo ndi amiyala opangidwa ndi anthu, nchifukwa chake adaiwononga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaponya milungu yao pamoto; pakuti iyo sinali milungu, koma ntchito yopangidwa ndi manja a anthu, mtengo ndi mwala; chifukwa chake iwo anaiononga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anaponyera pa moto milungu yawo ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mafano a mitengo ndi miyala, yopangidwa ndi manja a anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaponya milungu yao pamoto; pakuti iyo sinali milungu, koma nchito yopangidwa ndi manja a anthu, mtengo ndi mwala; cifukwa cace iwo anaiononga,