Isaiah 37:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye Inu Chauta, Mulungu wathu, mutipulumutse ife kwa munthu ameneyu, kuti mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziŵe kuti Inu nokha, Chauta, ndiye Mulungu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake, Yehova, Mulungu wathu, mutipulumutse ife m'manja mwake, kuti maufumu onse a dziko adziwe, kuti Inu ndinu Yehova, Inu nokha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni mʼdzanja lake kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndiye Mulungu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace, Yehova, Mulungu wathu, mutipulumutse ife m'manja mwace, kuti maufumu onse a dziko adziwe, kuti Inu ndinu Yehova, Inu nokha.