Isaiah 37:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Poitsutsa za mfumuyo Chauta adati, “Mzinda wa Ziyoni ukukunyoza ndi kukuseka, iwe Senakeribu, mzinda wa Yerusalemu ukupukusa mutu kumbuyo kwako monyodola.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
awa ndiwo mau amene Yehova wanena za iye, Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza iwe ndi kuseka iwe ndi chiphwete; mwana wamkazi wa Yerusalemu wapukusa mutu wake pambuyo pako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mawu amene Yehova wayankhula motsutsana naye ndi awa: “Mwana wamkazi wa Ziyoni akukunyoza ndi kukuseka. Mwana wamkazi wa Yerusalemu, akupukusa mutu wake pamene iwe ukuthawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
awa ndiwo mau amene Yehova wanena za iye, Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza iwe ndi kuseka iwe ndi ciphwete; mwana wamkazi wa Yerusalemu wapukusa mutu wace pambuyo pako.