Isaiah 37:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udatuma atumiki ako kudzanyoza Ine, ndipo udati, ‘Ndi magaleta anga ochuluka ndidakwera mapiri ataliatali, ndidafika mpaka pa nsonga za mapiri a ku Lebanoni. Ndidagwetsa mitengo yake ya mkungudza yaitali kwambiri, ndiponso mitengo yake ya paini yabwino koposa. Ndidaloŵanso m'kati mwake mwenimweni, mwankhalango yake yoŵirira kwabasi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wamtonza Ambuye ndi atumiki ako, ndipo wati, Ndi khamu la magaleta anga ine ndafika kunsonga za mapiri, kumbali za Lebanoni; ndipo ndidzagwetsapo mikungudza yaitali, ndi milombwa yosankhika; ndipo ine ndidzafika pamutu pake penipeni, kunkhalango ya munda wake wobalitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kudzera mwa amithenga ako iwe wanyoza Ambuye. Ndipo wanena kuti, ‘Ndi magaleta anga ochuluka ndafika pamwamba pa mapiri, pamwamba penipeni pa mapiri a Lebanoni. Ndagwetsa mitengo yamkungudza yayitali kwambiri, ndi mitengo yabwino kwambiri ya payini. Ndafika pa msonga pake penipeni, nkhalango yake yowirira kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wamtonza Ambuye ndi atumiki ako, ndipo wati, Ndi khamu la magareta anga ine ndafika ku nsonga za mapiri, ku mbali za Lebano; ndipo ndidzagwetsapo mikungudza yaitali, ndi milombwa yosankhika; ndipo ine ndidzafika pamutu pace penipeni, ku nkhalango ya munda wace wobalitsa.