Isaiah 37:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma Ine Chauta ndikuti, Kodi sudamvepo kuti zimenezi ndidazikonzeratu kalekale? Ndidaaziganiziratu masiku amakedzana. Tsopano ndazichitadi. Iweyo kwako kunali kungogwetsa mizinda yamalinga ndi kuisandutsa miyulu ya miyala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi iwe sunamve, kuti ndinachita ichi kale, ndi kuchikonza nthawi zakale? Tsopano Ine ndachikwaniritsa, kuti iwe ukapasule midzi yamalinga, isanduke miunda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi sunamvepo kuti zimenezi ndinazikonzeratu kalekale? Ndinazikonzeratu masiku amakedzana; tsopano ndazichitadi, kuti iwe kwako nʼkusandutsa mizinda yotetezedwa kukhala milu ya miyala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi iwe sunamve, kuti ndinacita ici kale, ndi kucikonza nthawi zakale? tsopano Ine ndacikwaniritsa, kuti iwe ukapasule midzi yamalinga, isanduke miunda.