Isaiah 37:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amene ankakhala kumeneko anali opanda mphamvu, ankada nkhaŵa, ndipo adaasokonezeka. Anali ngati mbeu zam'munda, ngati udzu wanthete. Anali ngati udzu wapadenga, umene mphepo imauumitsa usanakule nkomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake okhalamo analefuka, naopsedwa, nathedwa nzeru; ananga udzu wa m'munda, ndi masamba awisi, ndi udzu wa pamachindwi, ndi munda wa tirigu asanakule.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu amene ankakhala kumeneko analibenso mphamvu, ankada nkhawa ndi kuchititsidwa manyazi. Anali ngati mbewu za mʼmunda, ngati udzu wanthete, ali ngati udzu omera pa denga, umene mphepo imawumitsa usanakule nʼkomwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace okhalamo analefuka, naopsedwa, nathedwa nzeru; ananga udzu wa in'munda, ndi masamba awisi, ndi udzu wa pamacindwi, ndi munda wa tirigu asanakule.