Isaiah 37:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chakuti udandikwiyira, ndipo kudzitukumula kwako kudamveka kwa Ine, ndidzakola mphuno yako ndi mbedza, ndi kuika chitsulo m'kamwa mwako. Ndidzakubweza pokuyendetsa m'njira yomwe udadzera pobwera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa cha kundikwiyira Ine kwako, ndi popeza kudzikweza kwako kwafika m'makutu mwanga. Ine ndidzaika mbedza yanga m'mphuno mwako, ndi chapakamwa changa m'milomo yako, ndipo ndidzakubweza iwe m'njira yomwe unadzerayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa umandikwiyira Ine ndi kuti mwano wako wamveka mʼmakutu anga, ndidzakola mphuno yako ndi mbedza ndikuyika chitsulo mʼkamwa mwako, ndipo ndidzakubweza pokuyendetsa njira yomwe unadzera pobwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ca kundikwiyira Ine kwako, ndi popeza kudzikweza kwako kwafika m'makutu mwanga. Ine ndidzaika mbedza yanga m'mphuno mwako, ndi capakamwa canga m'milomo yako, ndipo ndidzakubweza iwe m'njira yomwe unadzerayo.