Isaiah 37:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwowo adauza Yesaya mau a Hezekiya onena kuti, “Lero ndi tsiku la mavuto, la chilango ndi la manyazi. Tili ngati mkazi wapathupi amene ali pafupi kubala mwana, koma alibe mphamvu zomubalira mwanayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo anati kwa iye, Hezekiya atere, Tsiku lalero ndilo tsiku la vuto, ndi lakudzudzula ndi chitonzo; pakuti nthawi yake yakubala ana yafika, ndipo palibe mphamvu yobalira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anamuwuza kuti, “Hezekiya akunena kuti, ‘Lero ndi tsiku lamavuto, lachilango ndi lamanyazi. Ife lero tili ngati mayi woyembekezera amene pofika nthawi yoti achire akupezeka kuti alibe mphamvu zoberekera.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo anati kwa iye, Hezekiya atere, Tsiku lalero ndilo tsiku la bvuto, ndi lakudzudzula, ndi citonzo; pakuti nthawi yace yakubala ana yafika, ndipo palibe mphamvu yobalira.