Isaiah 37:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Zimene akunena Chauta za mfumu ya ku Asiriya, ndiizi, akuti, ‘Sadzaloŵa mu mzinda umenewu, sadzaponyamo muvi ndi umodzi womwe. Ankhondo ake azishango sadzafika pafupi ndi mzinda umenewu, ndipo sadzauzinga ndi mtumbira wankhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Yehova za mfumu ya Asiriya, Iye sadzafika pa mudzi uno, ngakhale kuponyapo muvi, ngakhale kufika patsogolo pake ndi chikopa, ngakhale kuunjikirapo mulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Choncho Yehova akunena izi za mfumu ya ku Asiriya: “Iye sadzalowa mu mzinda umenewu kapena kuponyamo muvi uliwonse. Sadzafika pafupi ndi mzindawu ndi ankhondo ake a zishango kapena kuwuzinga ndi mitumbira yankhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Yehova za mfumu ya Asuri, Iye sadzafika pa mudzi uno, ngakhale kuponyapo mubvi, ngakhale kufika patsogolo pace ndi cikopa, ngakhale kuunjikirapo mulu.