Isaiah 37:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mngelo wa Chauta adapita ku zithando zankhondo za Aasiriya, naphako asilikali 185,000. M'maŵa mwake anthu adangoona asilikaliwo ali ngundangunda, atafa onsewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mthenga wa Yehova anatuluka, naphaipha m'zithando za Asiriya, zikwi zana ndi makumi asanu ndi atatu ndi zisanu, ndipo pamene anthu anauka mamawa, taonani, onse ndiwo mitembo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya nkhondo ya ku Asiriya ndikukapha asilikali 185,000. Podzuka mmawa mwake anthu anangoona mitembo ponseponse!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mthenga wa Yehova anaturuka, naphaipha m'zitando za Asuri, zikwi zana ndi makumi asanu ndi atatu ndi zisanu, ndipo pamene anthu anauka mamawa, taonani, onse ndiwo mitembo.