Isaiah 37:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina pamene ankapembedza m'nyumba ya Nisiroki, mulungu wake, ana ake aŵiri, Adrameleki ndi Sarezere, adamupha ndi malupanga ao, nathaŵira ku dziko la Ararati. Ndipo Esarahadoni, mwana wake wina, adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali, pamene iye analikupembedzera m'nyumba ya Nisiroki, mulungu wake, Adrameleki ndi Sarezere, ana ake anamupha iye ndi lupanga; ndipo iwo anapulumuka, nathawira ku dziko la ku Ararati. Ndipo Esarahadoni, mwana wake, analamulira m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina, pamene ankapembedza mʼnyumba ya mulungu wake, Nisiroki, ana ake awiri, Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga, ndipo anathawira mʼdziko la Ararati. Ndipo mwana wake Esrahadoni analowa ufumu mʼmalo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali, pamene iye analikupembedzera m'nyumba ya Nisiroki, mulungu wace, Adrameleki ndi Sarezeri, ana ace anampha iye ndi lupanga; ndipo iwo anapulumuka, nathawira ku dziko la ku Ararati. Ndipo Esaradoni, mwana wace, analamulira m'malo mwace.