Isaiah 37:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono pamene mfumu ya ku Asiriya idamva kuti mfumu Tirihaka wa ku Etiopiya akubwera kudzachita nayo nkhondo, idatumanso amithenga kwa mfumu Hezekiya ndi mau onena kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamva anthu alinkunena za Tirihaka, mfumu ya Kusi, Iye watuluka kudzamenyana ndi iwe. Ndipo pamene anamva, iye anatumiza mithenga kwa Hezekiya ndi kuti,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyi Senakeribu analandira uthenga wakuti Tirihaka, mfumu ya ku Kusi akubwera kudzachita naye nkhondo. Atamva zimenezi, anatumiza amithenga kwa Hezekiya ndi mawu awa:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamva anthu alinkunena za Tiraka, mfumu ya Kusi, Iye waturuka kudzamenyana ndi iwe. Ndipo pamene anamva, iye anatumiza mithenga kwa Hezekiya ndi kuti,