Isaiah 38:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo mfumu Hezekiya adaadwala, ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya, mwana wa Amozi, adapita kukamuwona, namuuza kuti, “Chauta akuti ukonze zonse bwino lomwe, poti ufa, suchira ai.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku amenewo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Ndipo Yesaya mneneri, mwana wa Amozi, anadza kwa iye, nati kwa iye, Atero Yehova, Konza nyumba yako, pakuti iwe udzafa, sudzakhala ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyo Mfumu Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya mwana wa Amozi anapita kukamuona ndipo anati “Yehova akuti: Konza bwino nyumba yako, pakuti ukufa; suchira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku amenewo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Ndipo Yesaya mneneri, mwana wa Amozi, anadza kwa iye, nati kwa iye, Atero Yehova, Konza nyumba yako, pakuti iwe udzafa, sudzakhala ndi moyo.