Isaiah 38:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Usiku wonse mpaka m'maŵa ndinkalira ndi ululu. Munkaphwanya mafupa anga onse, monga umachitira mkango. Kuyambira m'maŵa mpaka usiku mwakhala mukunditsiriza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinadzitonthoza kufikira mamawa; monga mkango, momwemo Iye anathyolathyola mafupa anga onse; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinkalira kupempha chithandizo usiku wonse mpaka mmawa; koma Inu Yehova munaphwanya mafupa anga ngati mkango, ndipo mwakhala mukundisiya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinadzitonthoza kufikira mamawa; monga mkango, momwemo Iye anatyolatyola mafupa anga onse; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.