Isaiah 38:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimene ndidamvera zoŵaŵa nkuti ndipeze bwino. Mwapulumutsa moyo wanga ku manda, mwataya machimo anga onse kumbuyo kwanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m'dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu machimo anga onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndithudi, ine ndinamva zowawa zotere kuti ndikhale ndi moyo; Inu munandisunga kuti ndisapite ku dzenje la chiwonongeko chifukwa mwakhululukira machimo anga onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, ndinali ndi zowawa zazikuru, Cifukwa ca mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, Munaupulumutsa m'dzanja la cibvundi, Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu macimo anga onse.