Isaiah 38:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Inu Chauta, mukumbukire kuti ndakhala ndikukutumikirani mokhulupirika ndi modzipereka. Ndipo nthaŵi zonse ndinali kuchita zokukomerani.” Atatero adayamba kulira ndi mtima woŵaŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kumbukiranitu tsopano, Yehova, kuti ndayenda pamaso panu m'zoonadi ndi mtima wangwiro, ndipo ndachita zabwino pamaso panu. Ndipo Hezekiya analira kolimba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu Yehova, kumbukirani momwe ndayendera pamaso panu mokhulupirika ndi modzipereka ndipo ndakhala ndikuchita zabwino pamaso panu.” Ndipo Hezekiya analira mosweka mtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kumbukiranitu tsopano, Yehova, kuti ndayenda pamaso panu m'zoonadi ndi mtima wangwiro, ndipo ndacita zabwino pamaso panu. Ndipo Hezekiya analira kolimba.