Isaiah 38:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesaya adauza Hezekiya kuti, “Chauta adzakupatsani chizindikiro kutsimikiza kuti adzasunga lonjezo lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe chochokera kwa Yehova, kuti Yehova adzachita ichi wanenachi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ichi ndi chizindikiro cha Yehova kwa iwe kutsimikiza kuti Yehova adzachita zimene walonjeza:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ici cidzakhala cizindikilo kwa iwe cocokera kwa Yehova, kuti Yehova adzacita ici wanenaci;