Isaiah 39:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani, mfumu ya ku Babiloni, adatuma amithenga naŵapatsira makalata ndi mphatso kuti akapereke kwa Hezekiya, poti adaamva kuti ankadwala ndipo adachira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nthawi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani, mfumu ya ku Babiloni, anatumiza akalata ndi mphatso kwa Hezekiya; pakuti anamva kuti iye anadwala, nachira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani mfumu ya ku Babuloni anatumiza nthumwi kwa Hezekiya nawapatsira makalata ndi mphatso, pakuti anamva za kudwala kwake ndi kuti anachira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nthawi imeneyo Merodakibaladani, mwana wa Baladani, mfumu ya ku Babulo, anatumiza akalata ndi mphatso kwa Hezekiya; pakuti anamva kuti iye anadwala, nacira.