Isaiah 39:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hezekiya adaŵalandira anthuwo, naŵaonetsa nyumba yosungiramo zinthu zake, monga siliva, golide, zokometsera chakudya, mafuta onunkhira amtengowapatali, zida zonse zankhondo ndiponso zonse zimene ankazisunga m'nyumba zake zosungiramo chuma. Panalibe kanthu kalikonse m'nyumbamo ndi mu ufumu wake wonse kamene sadaŵaonetse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hezekiya anakondwera nao, nawaonetsa nyumba yake ya chuma, siliva, ndi golide, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsera, ndi nyumba yonse ya zida zake, ndi zonse zopezedwa m'zosungira zake; munalibe kanthu m'nyumba mwake, kapena m'dziko lake lonse, kamene Hezekiya sanawaonetse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hezekiya anawalandira mwasangala ndipo anawaonetsa zonse zimene zinali mʼnyumba zake zosungiramo siliva, golide, zokometsera zakudya, mafuta abwino kwambiri, zida zonse zankhondo ndiponso zonse zimene zinkapezeka mʼnyumba zake zosungiramo chuma. Panalibe kanthu kalikonse ka mʼnyumba yaufumu kapena mu ufumu wake onse kamene sanawaonetse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hezekiya anakondwera nao, nawaonetsa nyumba yace ya cuma, siliva, ndi golidi, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsetsa, ndi nyumba yonse ya zida zace, ndi zonse zopezedwa m'zosungira zace; munalibe kanthu m'nyumba mwace, kapena m'dziko lace lonse, kamene Hezekiya sanawaonetsa.