Isaiah 39:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesaya adamufunsanso kuti, “Kodi m'nyumba mwanumo adaona chiyani?” Hezekiya adayankha kuti, “Adaona za m'nyumba mwanga. Palibe ndi chimodzi chomwe chimene sindidaŵaonetse m'nyumba zanga zosungiramo chuma.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anati, Kodi iwo anaona chiyani m'nyumba mwanu? Ndipo Hezekiya anayankha, Zonse za m'nyumba mwanga iwo anaziona; palibe kanthu ka mwa chuma changa, kamene ine sindinawaonetse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mneneri anafunsanso kuti, “Kodi mʼnyumba yanu yaufumu anaonamo chiyani?” Hezekiya anati, “Anaona chilichonse cha mʼnyumba yanga yaufumu. Palibe ndi chimodzi chomwe za mʼnyumba yosungiramo chuma changa chimene sindinawaonetse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anati, Kodi iwo anaona ciani m'nyumba mwanu? Ndipo Hezekiya anayankha, Zonse za m'nyumba mwanga iwo anaziona; palibe kanthu ka mwa cuma canga, kamene ine sindinawaonetse.