Isaiah 39:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumu Hezekiya adauza Yesaya kuti “mau amene Chauta walankhulaŵa ndi abwino.” Ponena zimenezo, ankaganiza kuti, “Palibe kanthu ai, malinga kuti padzakhale mtendere ndi bata masiku onse a moyo wanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova, amene iwe wanena, ali abwino. Iye anatinso, Pakuti padzakhala mtendere ndi zoonadi masiku anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hezekiya anayankha kuti, “Mawu a Yehova amene mwayankhula ndi abwino.” Ponena izi iye ankaganiza kuti, “Padzakhala mtendere ndi chitetezo masiku a moyo wanga onse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova, amene iwe wanena, ali abwino. Iye anatinso, Pakuti padzakhala mtendere ndi zoonadi masiku anga.