Isaiah 4:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo akazi asanu ndi aŵiri adzagwira mwamuna mmodzi, nkunena kuti, “Ife tizidya chakudya chathuchathu nkumavala zovala zathu; inu mungotilola tizitchulidwa akazi anu, kuti manyazi aumbeta atichoke.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akazi asanu ndi awiri adzagwira mwamuna mmodzi tsiku limenelo, nati, Ife tidzadya chakudya chathuchathu ndi kuvala zovala zathuzathu; koma titchedwe dzina lako; chotsa chitonzo chathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo akazi asanu ndi awiri adzagwira mwamuna mmodzi, nʼkunena kuti, “Ife tizidya chakudya chathuchathu, ndi kuvala zovala zathu; inu mungotilola kuti tidziyitanidwa ndi dzina lanu. Tichotseni manyazi aumbeta!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akazi asanu ndi awiri adzagwira mwamuna mmodzi tsiku limenelo, nati, Ife tidzadya cakudya cathu cathu ndi kubvala zobvala zathu zathu; koma tichedwe dzina lako; cotsa citonzo cathu.