Isaiah 4:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono masana Chauta adzaika mtambo ndi utsi kuzungulira phiri lonse la Ziyoni, pamwamba pa anthu ake. Usiku adzaika malaŵi a moto oŵala. Pamwamba pa zonse padzakhala ulemerero wa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova adzalenga pokhala ponse pa phiri la Ziyoni, ndi pa masonkhano ake, mtambo ndi utsi usana, ndi kung'azimira kwa malawi a moto usiku; chifukwa kuti pa ulemerero wonse padzayalidwa chophimba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yehova adzayika mtambo wake pamwamba ponse pa phiri la Ziyoni, ndipo pa onse amene asonkhana masana padzakhala mtambo wa utsi ndipo usiku padzakhala malawi amoto. Pamwamba pa zonse padzakhala ulemerero wa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova adzalenga pokhala ponse pa phiri la Ziyoni, ndi pa masonkhano ace, mtambo ndi utsi usana, ndi kung'azimira kwa malawi a moto usiku; cifukwa kuti pa ulemerero wonse padzayalidwa cophimba.