Isaiah 40:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye adzadyetsa zoweta chake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa pachepa pake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye adzasamalira nkhosa zake ngati mʼbusa: Iye adzasonkhanitsa ana ankhosa aakazi mʼmanja mwake ndipo Iye akuwanyamula pachifuwa chake ndi kutsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye adzadyetsa zoweta zace ngati mbusa, nadzasonkhanitsa ana a nkhosa pacapa pace, nadzawatengera pa cifuwa cace, ndipo adzatsogolera bwino bwino zimene ziyamwitsa.