Isaiah 40:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ndani adayesa kuchuluka kwa madzi am'nyanja ndi chikhatho chake, kapena kuyesa kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake? Ndani adayesa dothi lonse la dziko lapansi ndi dengu? Ndani adayesa kulemera kwa mapiri ndi magomo pa sikelo?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndani wayesa madzi m'dzanja lake, nayesa thambo ndi chikhato, ndi kudzaza fumbi la nthaka m'nsengwa, ndi kuyesa mapiri m'mbale zoyesera, ndi zitunda m'mulingo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi ndani akhoza kuyeza kuchuluka kwa madzi a mʼnyanja ndi chikhatho chake, kapena kuyeza kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake? Ndani akhoza kuyeza dothi lonse la dziko lapansi mʼdengu, kapena kuyeza kulemera kwa mapiri ndi zitunda ndi pasikelo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndani wayesa madzi m'dzanja lace, nayesa thambo ndi cikhato, ndi kudzaza pfumbi la nthaka m'nsengwa, ndi kuyesa mapiri m'mbale zoyesera, ndi zitunda m'mulingo?