Isaiah 40:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi Chauta adapemphapo nzeru kwa yani, kuti adziŵe zinthu? Ndani adamuphunzitsa kuweruza molungama? Ndani adamphunzitsa kudziŵa zinthu? Ndani adamlangiza njira ya kumvetsa zinthu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye anakhala upo ndi yani, ndipo ndani analangiza Iye ndi kumphunzitsa m'njira ya chiweruzo, ndi kumphunzitsa nzeru ndi kumuonetsa njira ya luntha?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi Yehova anapemphapo nzeru kwa yani kuti akhale wopenya, kapena kuti aphunzire njira yoyenera ndi nzeru? Iye anapempha nzeru kwa yani ndi njira ya kumvetsa zinthu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye anakhala upo ndi yani, ndipo ndani analangiza Iye ndi kumphunzitsa m'njira ya ciweruzo, ndi kumphunzitsa nzeru ndi kumuonetsa njira ya luntha?