Isaiah 40:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mitundu yonse ya anthu si kanthu konse pamaso pa Chauta, Iye amaziyesa zachabe ndi zopandapake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amitundu onse ali chabe pamaso pa Iye; awayesa ngati chinthu chachabe, ndi chopanda pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamaso pa Yehova mitundu yonse ya anthu ili ngati chinthu chopandapake; Iye amayiwerengera ngati chinthu chopanda phindu ndi cha chabechabe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amitundu onse ali cabe pamaso pa Iye; awayesa ngati cinthu cacabe, ndi copanda pace,