Isaiah 40:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko lapansi lidalengedwa ndi Iye amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba, kuseri kwa mlengalenga. Amaona anthu pansi ngati ziwala. Adafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchingira, ngati hema lokhalamo anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati chinsalu, naliyala monga hema wakukhalamo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba ndiye analenga dziko lapansi, Iye amaona anthu a dziko lapansi ngati ziwala. Ndipo anafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchinga, nayikunga ngati tenti yokhalamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekerezo a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati cinsaru, naliyala monga hema wakukhalamo;